Mavesi a m'Baibulo Onena za Chitetezo

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Chitetezo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 91:1-2

Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse. Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimadalira.”

02 Masalimo 121:7-8

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.

03 Yesaya 41:10

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

04 2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo.

05 Masalimo 32:7

Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. Sela

06 Masalimo 121:1-3

Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera.

07 Miyambo 18:10

Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.

Mitu yofanana