Mavesi a m'Baibulo Onena za Palibe Chida Chidzapindula
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Palibe Chida Chidzapindula oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke, ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa. Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova. Chipambano chawo chichokera kwa Ine,” akutero Yehova.
Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni: Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse. Sudzakhalanso ndi mantha chifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe.
Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndi linga la moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani? Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane kudzadya mnofu wanga, pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo, iwo adzapunthwa ndi kugwa.
“Onse amene akupsera mtima adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa; onse amene akukangana nawe sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Anthu 1,000 atha kufa pambali pako, anthu 10,000 kudzanja lako lamanja, koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.
Yehova adzaonetsetsa kuti adani anu amene adzakuwukirani agonjetsedwe pamaso panu. Iwo adzabwera kwa inu kuchokera mbali imodzi koma adzakuthawani ku mbali zisanu ndi ziwiri.
Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.”
Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”