Mavesi a m'Baibulo Onena za Nkhondo Yauzimu
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Nkhondo Yauzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga.
Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa.
Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga. Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.
Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.
Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.