Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Chishango Chathu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mulungu Chishango Chathu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

02 Genesis 15:1

Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati: “Usaope Abramu. Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yayikulu.”

03 Masalimo 3:3

Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.

04 Masalimo 18:30

Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa Iye.

05 Miyambo 30:5

“Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika; Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.

06 Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.

07 Masalimo 33:20

Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.

08 Masalimo 119:114

Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

Mitu yofanana