Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuponderezana

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kuponderezana oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yesaya 1:17

phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”

02 Masalimo 9:9

Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.

03 Masalimo 103:6

Yehova amachita chilungamo ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.

04 Mlaliki 4:1

Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano: ndinaona misozi ya anthu opsinjika, ndipo iwo alibe owatonthoza; mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo ndipo iwonso analibe owatonthoza.

05 Zekariya 7:10

Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’

06 Miyambo 22:22-23

Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu, pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.

07 Masalimo 12:5

“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.”

08 Masalimo 72:4

Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo.

09 Yesaya 10:1-2

Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo, kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.

10 Miyambo 14:31

Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

11 Masalimo 146:7

Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala. Yehova amamasula amʼndende,

12 Yeremiya 22:3

Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.

13 Amosi 5:11

Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake.

Mitu yofanana