Mavesi a m'Baibulo Onena za Chilungamo
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Chilungamo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!
Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni.
Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama; dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima, iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo. Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.
Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.
Odala ndi amene amasunga chilungamo, amene amachita zolungama nthawi zonse.