Mavesi a m'Baibulo Onena za Mlendo

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mlendo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Levitiko 19:34

Mlendo amene akhala nanu akhale ngati mmodzi mwa mbadwa zanu. Mumukonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Paja inu munali alendo mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

02 Eksodo 23:9

“Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.

03 Deuteronomo 10:19

Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto.

04 Ahebri 13:2

Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa.

05 Mateyu 25:35

Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira,

06 Levitiko 19:33

“ ‘Pamene mlendo akhala nanu mʼdziko mwanu, musamuzunze.

07 Numeri 15:15-16

Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’ ”

08 Deuteronomo 24:14

Osamapezera mwayi pa anthu aganyu osauka ndi aumphawi, kaya ndi Mwisraeli kapena mlendo wokhala mu umodzi mwa mizinda yanu.

Mitu yofanana