Mavesi a m'Baibulo Onena za Mkazi Wamasiye
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Mkazi Wamasiye oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala.
phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
“Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.
Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse.
Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha.
‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza. Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”
Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’
Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.
Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, “Usalire.”
kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.
Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama. Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa.