Mavesi a m'Baibulo Onena za Mwana Wamasiye
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mwana Wamasiye oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala.
Asiriya sangatipulumutse; ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo, sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’ kwa zimene manja athu omwe anazipanga, pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”
Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa, mumaganizira zochitapo kanthu. Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
“Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.
‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza. Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”
phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
Musachitire mlendo kapena mwana wamasiye zoyipa, kapena kulanda mkazi wamasiye chovala ngati chikole cha ngongole.
Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya Yehova adzandisamala.
Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’