Mavesi a m'Baibulo Onena za Osauka

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Osauka oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 19:17

Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

02 Miyambo 14:31

Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

03 Masalimo 41:1

Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

04 Agalatiya 2:10

Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.

05 Miyambo 28:27

Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

06 Masalimo 140:12

Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.

07 Luka 14:13

Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona.

08 Miyambo 22:9

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

09 Miyambo 29:7

Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.

10 Deuteronomo 15:7-8

Ngati pali mʼbale wanu wina wosauka mu mzinda wanu wina uliwonse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musawumitse mitima yanu kapena kuchita kaligwiritsa kwa mʼbale wanu wosaukayo. Koma mukhale ofewa manja ndipo mumukongoze mʼbale wanu momasuka pa chilichonse chimene akufuna.

11 Masalimo 113:7

Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;

12 Luka 4:18

“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,

13 Yakobo 2:5

Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?

14 Miyambo 31:9

Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.

Mitu yofanana