Mavesi a m'Baibulo Onena za Kutchinjiriza Ofooka

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kutchinjiriza Ofooka oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 82:3

Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.

02 Miyambo 31:8-9

Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera. Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.

03 Yesaya 1:17

phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”

04 Masalimo 72:4

Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo.

05 Yeremiya 22:3

Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.

06 Masalimo 82:4

Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

07 Miyambo 24:11-12

Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe; uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa. Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?

08 Yesaya 1:23

Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.

09 Deuteronomo 27:19

“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

10 Masalimo 41:1

Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

Mitu yofanana