Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudalira Ulamuliro Wake

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kudalira Ulamuliro Wake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 16:9

Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.

02 Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

03 Masalimo 37:5

Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:

04 Yeremiya 10:23

Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake; munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.

05 Yesaya 26:3

Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.

06 Masalimo 56:3-4

Ndikachita mantha ndimadalira Inu. Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda, mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha. Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?

07 Nahumu 1:7

Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,

08 Masalimo 9:10

Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

09 Yesaya 41:10

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mitu yofanana