Mavesi a m'Baibulo Onena za Nthawi ya Mulungu
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Nthawi ya Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake, ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.
Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, wobadwa mwa mayi, wobadwa pansi pa lamulo,
Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake; masomphenyawa akunena zamʼtsogolo ndipo sizidzalephera kuchitika. Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere; zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.
“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova. “Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.