Mavesi a m'Baibulo Onena za Ulamuliro wa Mulungu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Ulamuliro wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 103:19

Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.

02 Masalimo 47:8

Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.

03 Danieli 4:35

Anthu onse a dziko lapansi ali chabe pamaso pake. Pakati pa angelo akumwamba ndi anthu a dziko lapansi palibe amene akhoza kumuletsa Mulungu kuchita zimene afuna. Kapena kunena kwa Iye kuti, “Kodi mwachita chiyani?”

04 1 Mbiri 29:11-12

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.

05 Masalimo 22:28

pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.

06 Masalimo 115:3

Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.

07 Danieli 4:34

Pomaliza pa zaka zimenezo ine, Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndipo nzeru zanga zinabwereramo. Kenaka ndinatamanda Wammwambamwamba; ndinamupatsa ulemu ndi kumulemekeza Iye amene akhala nthawi zonse. Ulamuliro wake ndi ulamuliro wa nthawi zonse; ufumu wake udzakhala ku mibadomibado.

08 Masalimo 96:10

Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.” Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe; Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.

09 Yesaya 40:15

Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko. Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo; mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.

10 Masalimo 145:13

Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.

11 Aefeso 1:11

Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,

Mitu yofanana