Mavesi a m'Baibulo Onena za Palibe Chosatheka
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Palibe Chosatheka oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”
Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”
“Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani.
Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.”
Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”
“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse; chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife,
Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”
Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.”
Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.
Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa, kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.
Kenaka Asa anafuwulira Yehova Mulungu wake ndipo anati “Yehova palibe wina wofanana nanu kuti angathandize anthu opanda mphamvu pakati pa amphamvu. Tithandizeni Inu Yehova Mulungu wathu pakuti ife timadalira Inu ndipo mʼdzina lanu ife tabwera kudzalimbana ndi gulu la ankhondo lalikulu kwambiri ngati ili. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu, musalole kuti munthu akupambaneni.”