Mavesi a m'Baibulo Onena za Ulamuliro ndi Kusamalira kwa Mulungu
Palibe chimene chili kunja kwa ulamuliro wa Mulungu; Iye amachita zinthu zonse mogwirizana ndi cholinga cha chifuniro chake. Tikudziwa kuti zinthu zonse zimagwirira ntchito pamodzi kuti zikhale zabwino kwa iwo amene amakonda Mulungu. Mavesi awa amakhazikitsa mtima mu ulamuliro wa Mulungu wanzeru ndi wachikondi pa mbali iliyonse ya moyo.
Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.
Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.
Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.
Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake, ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.
Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,
Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova, tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?
Masiku anga ali mʼmanja mwanu; ndipulumutseni kwa adani anga ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.