Mavesi a m'Baibulo Onena za Masiku Athu Ali M'manja Mwake

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Masiku Athu Ali M'manja Mwake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 31:15

Masiku anga ali mʼmanja mwanu; ndipulumutseni kwa adani anga ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.

02 Masalimo 139:16

Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

03 Yobu 14:5

Masiku a munthu ndi odziwikiratu; munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.

‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’

05 Masalimo 90:12

Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

06 Yakobo 4:13-15

Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.” Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.”

07 Deuteronomo 32:39

“Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo! Palibe mulungu wina koma Ine ndekha. Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo, ndavulaza ndipo ndidzachiritsa, ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.

Mitu yofanana