Mavesi a m'Baibulo Onena za Wowumba ndi Dongo
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Wowumba ndi Dongo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
“Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.
Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ” Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?
Inu mumazondotsa zinthu ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya. Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti “Sunandipange ndi iwe?” Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti, “Iwe sudziwa chilichonse?”
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
“Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga? Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?
“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake, ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti, ‘Kodi ukuwumba chiyani?’ Kodi ntchito yako inganene kuti, ‘Ulibe luso?’
Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.
Kodi mukumubwezera Yehova chotere, inu anthu opusa ndi opanda nzeru? Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu, amene anakupangani ndi kukuwumbani?
Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo.
Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi.
onsewo amadziwika ndi dzina langa; ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndinawawumba, inde ndinawapanga.”