Mavesi a m'Baibulo Onena za Zolinga Zake Zimakhazikika

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Zolinga Zake Zimakhazikika oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yesaya 46:10

Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.

02 Miyambo 19:21

Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

03 Yobu 42:2

“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse; chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.

04 Masalimo 33:11

Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

05 Yesaya 14:24

Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti, “Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho, ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.

06 Yobu 23:13

“Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye? Iye amachita chilichonse chimene wafuna.

Mitu yofanana