Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Amagwira Ntchito Zonse

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Mulungu Amagwira Ntchito Zonse oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 1:11

Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,

02 Aroma 8:28

Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.

03 Akolose 1:16-17

Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye.

04 Masalimo 135:6

Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.

05 Danieli 2:21

Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.

06 Yesaya 46:10

Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.

07 Miyambo 16:4

Yehova amachita zonse ndi cholinga chake, ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.

08 Aroma 11:36

Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

09 Masalimo 33:11

Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

Mitu yofanana