Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusamalira kwa Mulungu
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kusamalira kwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?
Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi.
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.
Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,
Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.
Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu, ndi zosawerengeka ndithu! Ndikanaziwerenga, zikanakhala zochuluka kuposa mchenga; pamene ndadzuka, ndili nanube.
Za fuko la Benjamini anati: “Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye, pakuti amamuteteza tsiku lonse, ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”