Mavesi a m'Baibulo Onena za Chifundo

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Chifundo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 103:13

Monga bambo amachitira chifundo ana ake, choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;

02 Maliro 3:22-23

Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.

03 Masalimo 145:8

Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

04 Mateyu 9:36

Ataona maguluwo, anagwidwa ndi chisoni chifukwa anali ozunzika ndi osowa chithandizo ngati nkhosa zopanda mʼbusa.

05 Yesaya 49:15

“Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni? Ngakhale iye angathe kuyiwala, Ine sindidzakuyiwala iwe!

06 Masalimo 116:5

Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.

Mitu yofanana