Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukhulupirika kwa Mulungu

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kukhulupirika kwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Maliro 3:22-23

Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.

02 Deuteronomo 7:9

Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake.

03 1 Akorinto 1:9

Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.

04 2 Timoteyo 2:13

Ngati ndife osakhulupirika, Iye adzakhalabe wokhulupirika popeza sangathe kudzikana.

05 Masalimo 36:5

Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba, kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.

06 Masalimo 89:8

Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu? Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.

07 Ahebri 10:23

Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.

Mitu yofanana