Mavesi a m'Baibulo Onena za Ubwino wa Mulungu

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Ubwino wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 34:8

Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye.

02 Masalimo 100:5

Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

03 Masalimo 145:9

Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.

04 Nahumu 1:7

Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,

05 Aroma 8:32

Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere?

06 Masalimo 31:19

Ndi waukulu ubwino wanu umene mwawasungira amene amakuopani, umene mumapereka anthu akuona kwa iwo amene amathawira kwa Inu.

07 Masalimo 27:13

Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.

08 Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.

09 Masalimo 23:6

Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.

10 Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.

11 Masalimo 86:5

Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino, wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.

12 Eksodo 33:19

Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”

13 Masalimo 119:68

Inu ndinu abwino ndipo zimene mumachita ndi zabwino; phunzitseni malamulo anu.

14 Yeremiya 29:11

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

Mitu yofanana