Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuleza Mtima kwa Mulungu

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kuleza Mtima kwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 2 Petro 3:9

Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

02 Aroma 2:4

Kodi kapena ukupeputsa kukoma mtima kwa Mulungu, kuleza mtima kwake ndi kupirira kwake? Kodi sukuzindikira kuti kukoma mtima kwakeko, nʼkofuna kuti iweyo ulape machimo ako?

03 Eksodo 34:6

Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika,

04 1 Timoteyo 1:16

Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha.

05 Masalimo 86:15

Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.

06 Nehemiya 9:17

Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye.

Mitu yofanana