Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikondi cha Mulungu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Chikondi cha Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Yohane 4:10

Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.

02 Yohane 3:16

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

03 Aroma 5:8

Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

04 1 Yohane 3:1

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

05 Aroma 8:38-39

Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

06 Aefeso 3:18-19

kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.

07 1 Yohane 4:16

Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.

08 Zefaniya 3:17

Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”

Mitu yofanana