Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyenda Molungama
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Kuyenda Molungama oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.
Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera? Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa, amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.
Amene amayenda molungama amaopa Yehova, koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.
Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama; udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri.
Angathe kuti ndi amene amachita zolungama ndi kuyankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu, amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa. Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja, kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri. Azidzalandira chakudya chake ndipo madzi sadzamusowa.
Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
Chilungamo chimateteza munthu wangwiro, koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.