Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuona Mtima ndi Kuyera
Mulungu amayitana anthu ake kuti ayende ndi kukhulupirika ndi kusunga mitima yawo yoyera pamaso pake. Odala ali oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu. Mavesi awa amalimbikitsa moyo woyera ndi wosagawanika.
Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe.
Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.
Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika? Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo.
kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba
Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.
Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa.
Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona.
Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.