Mavesi a m'Baibulo Onena za Inde Wanu Akhale Inde

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Inde Wanu Akhale Inde oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 5:37

Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.

02 Yakobo 5:12

Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.

03 Masalimo 15:4

amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka,

04 Numeri 30:2

Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena.

05 Mlaliki 5:5

Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo.

06 Deuteronomo 23:23

Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu.

Mitu yofanana