Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuona Mtima

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Kuona Mtima oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 10:9

Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.

02 Miyambo 11:3

Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.

03 Masalimo 25:21

Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze, chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.

04 Yobu 27:5

Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona; mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.

05 Miyambo 20:7

Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.

06 Masalimo 26:1

Weruzeni Inu Yehova pakuti ndakhala moyo wosalakwa. Ndadalira Yehova popanda kugwedezeka.

07 Miyambo 19:1

Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.

08 Miyambo 28:6

Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.

09 Masalimo 41:12

Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.

10 1 Mbiri 29:17

Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu.

11 Miyambo 11:1

Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.

12 Tito 2:7

Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako.

13 Luka 16:10

“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.

14 Miyambo 21:3

Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.

15 Masalimo 78:72

Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama; ndi manja aluso anawatsogolera.

Mitu yofanana