Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyera kwa Mtundu wa Ukwati
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Kuyera kwa Mtundu wa Ukwati oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe.
Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu,
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.
Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi. Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.
Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu.
“Ndinachita pangano ndi maso anga kuti sindidzapenya namwali momusirira.
Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.
Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.
Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.
Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.