Mavesi a m'Baibulo Onena za Kunena Zoona

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kunena Zoona oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 12:22

Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.

02 Miyambo 11:1

Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.

03 Aefeso 4:25

Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi.

04 Zekariya 8:16

Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu;

05 2 Akorinto 8:21

Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.

06 Miyambo 16:13

Mawu owona amakondweretsa mfumu. Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.

07 Akolose 3:9

Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake

08 Levitiko 19:11

“ ‘Musabe. “ ‘Musamanamizane. “ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.

09 Miyambo 19:1

Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.

10 Ahebri 13:18

Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu.

11 Miyambo 24:26

Woyankhula mawu owona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.

12 Aroma 12:17

Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense.

13 Miyambo 20:23

Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.

14 Masalimo 34:13

asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.

Mitu yofanana