Mavesi a m'Baibulo Onena za Mtima Woyera

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Mtima Woyera oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 24:3-4

Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika? Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo.

02 Masalimo 51:10

Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.

03 Mateyu 5:8

Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.

04 Miyambo 4:23

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.

05 Yakobo 4:8

Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.

Mitu yofanana