Mavesi a m'Baibulo Onena za Mpando Wachifumu wa Mulungu
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mpando Wachifumu wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo.
Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.
Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo.
Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi; ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
“Ine ndikuyangʼanabe ndinaona “mipando yaufumu ikukhazikitsidwa, ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake. Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana; tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje. Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto, ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.
Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu.
Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo. Ndipo ankafuwula mokweza kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu, wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa.”
Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.
Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.