Mavesi a m'Baibulo Onena za Ulemerero Wake

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Ulemerero Wake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 19:1

Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake.

02 Yesaya 6:3

Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

03 Habakuku 2:14

Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.

04 Masalimo 96:3

Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

05 Numeri 14:21

Komabe, ndikunenetsa kuti pali Ine, ndiponso pamene dziko lapansi ladzaza ndi ulemerero wa Yehova,

06 Yesaya 42:8

“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.

07 Aroma 11:36

Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

08 Masalimo 72:19

Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni.

09 Eksodo 33:18

Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.”

10 Yesaya 40:5

Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera, ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona, pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”

11 1 Mbiri 16:24

Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.

12 Masalimo 57:5

Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba; mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Mitu yofanana