Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuchita Mantha pamaso pa Mulungu

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kuchita Mantha pamaso pa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 33:8

Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.

02 Masalimo 96:9

Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

03 Habakuku 2:20

Koma Yehova ali mʼNyumba yake yopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.”

04 Masalimo 89:7

Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.

05 Ahebri 12:28

Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha.

Mitu yofanana