Mavesi a m'Baibulo Onena za Ukulu Wake

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Ukulu Wake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 8:1

Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.

02 Masalimo 93:1

Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.

03 Masalimo 104:1

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu.

04 1 Mbiri 29:11

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

05 Yuda 1:25

kwa Mulungu yekhayo, Mpulumutsi wathu, kwa Iye kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, kuyambira isanayambe nthawi, tsopano mpaka muyaya. Ameni.

06 Masalimo 145:5

Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

07 Masalimo 96:6

Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

08 Deuteronomo 33:26

“Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni, amene amakwera pa thambo kukuthandizani ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.

09 Masalimo 21:5

Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.

10 2 Petro 1:16

Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake.

11 Masalimo 29:4

Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.

12 Yesaya 2:10

Lowani mʼmatanthwe, bisalani mʼmaenje, kuthawa kuopsa kwa Yehova ndi ulemerero wa ufumu wake!

Mitu yofanana