Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyera kwa Mulungu

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kuyera kwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yesaya 6:3

Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

02 1 Petro 1:15-16

Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.”

03 Levitiko 19:2

“Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.

04 Chivumbulutso 15:4

Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

05 1 Samueli 2:2

“Palibe wina woyera ngati Yehova, palibe wina koma inu nokha, palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

06 Habakuku 1:13

Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa; Inu simulekerera cholakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa? Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?

07 Masalimo 99:5

Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mulambireni pa mapazi ake; Iye ndi woyera.

08 Eksodo 15:11

Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa?

09 Yesaya 57:15

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

Mitu yofanana