Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuwala kwa Ulemerero wa Mulungu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Kuwala kwa Ulemerero wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Mbiri 29:11

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

02 Masalimo 104:1

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu.

03 Masalimo 96:6

Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

04 Masalimo 145:5

Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

05 Masalimo 8:1

Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.

06 Masalimo 21:5

Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.

07 Yobu 37:22

Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto; Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.

08 Masalimo 111:3

Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

09 Habakuku 3:3-4

Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani. Sela Ulemerero wake unaphimba mlengalenga ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake. Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa; kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake, mʼmene anabisamo mphamvu zake.

10 Masalimo 90:16

Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu, kukongola kwanu kwa ana awo.

11 Yesaya 60:1

“Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika, ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.

Mitu yofanana