Mavesi a m'Baibulo Onena za Banja

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Banja oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yoswa 24:15

Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova.”

02 Masalimo 127:1

Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe.

03 Miyambo 24:3-4

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu; Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.

04 Miyambo 14:1

Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.

Iwo anayankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako.”

06 Deuteronomo 6:9

Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

07 Miyambo 12:7

Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika, koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.

08 Miyambo 15:6

Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.

09 Masalimo 128:3

Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako.

10 Miyambo 31:27

Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.

11 1 Timoteyo 5:8

Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

12 Masalimo 101:2

Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa.

Mitu yofanana