Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulera Ana
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kulera Ana oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Mwana muzimuphunzitsa njira yake, ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana, koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.
Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita. Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli, zimene analamulira makolo athu kuphunzitsa ana awo, kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa, ngakhale ana amene sanabadwe, ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.
Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.
Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake, ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.
Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.