Mavesi a m'Baibulo Onena za Amuna ndi Akazi

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Amuna ndi Akazi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 5:25

Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo

02 1 Petro 3:7

Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.

03 Aefeso 5:33

Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.

04 Akolose 3:18-19

Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.

05 1 Akorinto 7:3

Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake.

06 1 Petro 3:1

Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu

07 Aefeso 5:28

Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha.

Mitu yofanana