Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikondi ndi Ulemu

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Chikondi ndi Ulemu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 5:33

Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.

02 Aefeso 5:25

Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo

03 1 Petro 3:1-2

Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu.

04 Akolose 3:19

Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.

05 1 Akorinto 13:4-5

Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa.

06 1 Petro 3:7

Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.

07 Aroma 12:10

Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni.

Mitu yofanana