Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulemekeza Makolo
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kulemekeza Makolo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.”
Mvera abambo ako amene anakubala, usanyoze amayi ako pamene akalamba.
Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
“ ‘Aliyense mwa inu azilemekeza abambo ake ndi amayi ake. Ndipo muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.