Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulera Ana Auzimu

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kulera Ana Auzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yake, ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

02 Deuteronomo 6:6-7

Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.

03 Aefeso 6:4

Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

04 Masalimo 78:4

Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.

05 Miyambo 29:17

Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.

06 Miyambo 22:15

Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana, koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

07 Miyambo 13:24

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.

08 2 Timoteyo 1:5

Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.

09 Miyambo 1:8-9

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako. Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.

10 Yesaya 54:13

Yehova adzaphunzitsa ana ako onse, ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.

11 Deuteronomo 4:9

Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo.

12 3 Yohane 1:4

Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.

Mitu yofanana