Mavesi a m'Baibulo Onena za Mkazi wa Khalidwe Labwino
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mkazi wa Khalidwe Labwino oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake; ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo. Iye amayankhula mwanzeru, amaphunzitsa anthu mwachikondi.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa; koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.
Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira ndipo mwamunayo sasowa phindu.
Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe. Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala; ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo; koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.
Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.
Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.