Mavesi a m'Baibulo Onena za Ukwati
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Ukwati oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.
“Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.
Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”
Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.
Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu. Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu.
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu: Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse!
Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake. Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake.
Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.