Mavesi a m'Baibulo Onena za Yendani mwa Nzeru

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Yendani mwa Nzeru oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Akolose 4:5

Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo.

02 Aefeso 5:15-16

Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.

03 Yakobo 1:5

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

04 Miyambo 4:7

Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.

05 Akolose 1:9-10

Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa. Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu.

06 Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

07 Miyambo 9:10

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

08 Yakobo 3:17

Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.

09 Masalimo 90:12

Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

10 Miyambo 2:6

Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.

Mitu yofanana