Mavesi a m'Baibulo Onena za Kupanga Zosankha

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kupanga Zosankha oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 16:9

Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.

02 Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

03 Yakobo 1:5

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

04 Miyambo 19:21

Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

05 Masalimo 37:23

Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu, amakhazikitsa mayendedwe ake;

06 Akolose 3:15

Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.

07 Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.

08 Miyambo 14:8

Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake. Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.

09 Luka 14:28

“Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?

Mitu yofanana