Mavesi a m'Baibulo Onena za Nzeru

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Nzeru oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yakobo 1:5

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

02 Miyambo 2:6

Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.

03 Miyambo 9:10

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

04 Akolose 2:3

Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso.

05 1 Akorinto 1:30

Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.

06 Miyambo 4:7

Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.

07 Yakobo 3:17

Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.

08 Mlaliki 7:12

Nzeru ndi chitetezo, monganso ndalama zili chitetezo, koma phindu la chidziwitso ndi ili: kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.

09 Miyambo 3:13

Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

10 Aefeso 5:15-16

Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.

11 Miyambo 16:16

Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

12 Danieli 2:21

Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.

13 Masalimo 111:10

Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

Mitu yofanana